Pular para o conteúdo
Publicidade

1 Akorinto 12:1-7

Mphatso za Mzimu Woyera

1 Tsopano abale anga okondedwa, sindikufuna mukhale osadziwa za mphatso za Mzimu. 2 Inu mukudziwa kuti pamene munali akunja, ankakusocheretsani mʼnjira zosiyanasiyana ndi kukukokerani ku mafano osayankhula. 3 Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti palibe munthu amene ali ndi Mzimu wa Mulungu angayankhule kuti, "Yesu atembereredwe," ndiponso palibe munthu anganene kuti "Yesu ndi Ambuye," popanda kutsogozedwa ndi Mzimu Woyera.

4 Pali mphatso zosiyanasiyana, koma Mzimu yemweyo. 5 Pali mautumiki osiyanasiyana koma Ambuye yemweyo. 6 Pali magwiridwe antchito osiyanasiyana, koma Mulungu yemweyo amagwira ntchito monsemo mwa anthu onse.

7 Tsono Mzimu amapereka mphatso kwa aliyense kuti ipindulire onse.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.