Pular para o conteúdo
Publicidade

1 Akorinto 13:1-7

Kupambana kwa Chikondi

1 Ngakhale nditamayankhula mʼmalilime a anthu ndi a angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chinganga chaphokoso kapena ngati chitsulo chosokosera. 2 Ngati ndili ndi mphatso ya uneneri, nʼkumazindikira zinsinsi ndi kudziwa zonse, ndipo ngati ndili ndi chikhulupiriro chosuntha mapiri, koma wopanda chikondi, ine sindili kanthu. 3 Ngati ndipereka zanga zonse kwa osauka ndi kupereka thupi langa kuti alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ine sindipindula kanthu.

4 Chikondi nʼcholeza mtima, chikondi nʼchokoma mtima, chilibe nsanje, sichidzikuza, sichidzitamandira. 5 Chikondi chilibe mwano, sichodzikonda, sichipsa mtima msanga, sichisunga mangawa. 6 Chikondi sichikondwera ndi zoyipa koma chimakondwera ndi choonadi. 7 Chimatchinjiriza nthawi zonse, chimakhulupirika nthawi zonse, chimakhala ndi chiyembekezo nthawi zonse, chimapirira nthawi zonse.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.