Pular para o conteúdo
Publicidade

1 Mbiri 29:11,12,14,15

11 Wanu, Inu Yehova ndi ukulu ndi mphamvu,

ulemerero ndiponso ufumu ndi kukongola.

Pakuti zinthu zonse zakumwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu.

Wanu, Inu Yehova ndi ufumu;

Inu ndinu wokwezeka ndipo ndinu mtsogoleri wa zonse.

12 Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu;

Inu ndinu wolamulira zinthu zonse.

Mʼdzanja lanu muli nyonga ndi mphamvu,

kukweza ndi kupereka nyonga kwa onse.

14 "Koma ine ndine yani, ndipo anthu anga ndani, kuti tikupatsani mowolowamanja motere? Zinthu zonse zimachokera kwa Inu, ndipo ife takupatsani zomwe zimachokera mʼdzanja lanu. 15 Ife ndife anthu osadziwika ndiponso alendo pamaso panu, monga analili makolo athu. Masiku anthu pa dziko lapansi ali ngati chithunzithunzi, wopanda chiyembekezo.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.