Pular para o conteúdo
Publicidade

1 Mafumu 19:19-21

Kuyitanidwa kwa Elisa

19 Kotero Eliya anachoka kumeneko, nakapeza Elisa mwana wa Safati. Iye ankatipula ndi mapulawo khumi ndi awiri okokedwa ndi ngʼombe ziwiriziwiri zapamagoli, ndipo iye mwini ankayendetsa goli la khumi ndi chiwiri. Eliya anapita kumene anali namuveka chofunda chake. 20 Pomwepo Elisa anasiya ngʼombe zake nathamangira Eliya. Iye anati, "Mundilole kuti ndikatsanzike abambo ndi amayi anga, ndipo kenaka ndidzakutsatani."

Eliya anayankha kuti, "Bwerera. Ine ndachita chiyani kwa iwe?"

21 Choncho Elisa anamusiya Eliyayo nabwerera kwawo. Anatenga ngʼombe zake ziwiri zapagoli nazipha. Anatenga magoli a mapulawo ake nasonkhera moto kuphikira nyamayo ndipo anayipereka kwa anthu kuti adye. Ndipo ananyamuka natsatira Eliya ndi kukhala mtumiki wake.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.