Pular para o conteúdo
Publicidade

1 Mafumu 19:9,11-13

9 Kumeneko analowa mʼphanga, nakhala komweko.

Ambuye Aonekera Eliya

Ndipo taonani, Yehova anayankhula naye kuti, "Eliya, ukuchita chiyani kuno?"

11 Yehova anati, "Tuluka ndipo ukayime pa phiri pamaso pa Yehova, pakuti Yehova ali pafupi kudutsa pamenepo."

Tsono mphepo yayikulu ndi yamphamvu inawomba ningʼamba mapiri ndi kuswa matanthwe pamaso pa Yehova, koma Yehova sanali mʼmphepomo. Itapita mphepoyo panachita chivomerezi, koma Yehova sanali mʼchivomerezicho. 12 Chitapita chivomerezicho, panafika moto, koma Yehova sanali mʼmotomo. Ndipo utapita motowo, panamveka kamphepo kayaziyazi. 13 Eliya atamva kamphepoko, anakokera chovala chake naphimba kumutu. Anatuluka ndipo anayima pa khomo la phanga.

Ndipo panamveka mawu akuti, "Eliya, ukuchita chiyani kuno?"

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.