Pular para o conteúdo
Publicidade

1 Samueli 17:4,33,37,40,45,49

4 Tsono munthu wina wamphamvu, dzina lake Goliati wochokera ku Gati anatuluka ku misasa ya Afilisti. Msinkhu wake unali pafupipafupi mamita atatu.

33 Sauli anayankha Davide kuti, "Iwe sungathe kupita kukamenyana ndi Mfilisitiyu. Iwe ukanali mnyamata, koma iyeyu ndi amene wakhala akumenya nkhondo kuyambira unyamata wake."

37 Yehova amene anandilanditsa mʼkamwa mwa mkango ndi chimbalangondo adzandilanditsa mʼmanja mwa Mfilisiti uyu."

Sauli anati kwa Davide, "Pita, ndipo Yehova akhale nawe."

40 Pambuyo pake anatenga ndodo yake mʼmanja. Kenaka anasankha miyala yosalala bwino mu mtsinje ndi kuyiika mʼthumba lake la ku ubusa. Legeni ili mʼmanja mwake, Davide ananyamuka kukakumana ndi Mfilisiti uja.

45 Koma Davide anati kwa Mfilisitiyo, "Iwe wabwera kwa ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo, koma ine ndikubwera kwa iwe mʼdzina la Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa ankhondo Aisraeli amene iwe ukuwanyoza.

49 Davideyo anapisa dzanja lake mʼthumba lake natengamo mwala ndipo anawuponya, nalasa pa mphumi pa Mfilisitiyo. Mwalawo unalowa pa chipumi chake, ndipo anagwa chafufumimba.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.