Pular para o conteúdo
Publicidade

1 Samueli 21:10-15

Davide ku Gati

10 Tsiku lomwelo Davide ananyamuka kuthawa Sauli ndipo anapita kwa Akisi, mfumu wa ku Gati. 11 Koma nduna za Akisi zinafunsa mfumuyo kuti, "Kodi uyu si Davide mfumu ya dzikoli? Kodi iyeyu si uja pomuvinira ankayimba kuti,

"Sauli wapha 1,000,

koma Davide wapha miyandamiyanda?"

12 Mawu amenewa anamulowa kwambiri Davide mu mtima ndipo anayamba kuopa kwambiri Akisi mfumu ya ku Gati. 13 Choncho anasintha makhalidwe ake pamaso pawo, nʼkudzisandutsa ngati wamisala. Iye ankangolembalemba pa zitseko za chipata ndi kumangotuluka dovi, nʼkumayenderera mʼndevu zake.

14 Akisi anawuza nduna zake kuti, "Mukumuona munthu uyu kuti ndi wamisala! Nʼchifukwa chiyani mukubwera naye kwa ine? 15 Kodi ine ndikusowa anthu amisala kuti muzibwera naye munthuyu kwa ine kuti azidzachita zamisala zake pamaso panga? Kodi munthu ameneyu nʼkulowa mʼnyumba mwanga?"

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.