3 Ndi mantha, Yehosafati anaganiza zofunsira kwa Yehova, ndipo analengeza kuti Ayuda onse asale zakudya. 4 Anthu a ku Yuda anabwera pamodzi kudzafuna thandizo kwa Yehova, ndipo anabweradi kuchokera ku mzinda uliwonse wa mu Yuda kudzafunafuna Yehova.
15 Iye anati, "Tamverani mfumu Yehosafati ndi onse amene amakhala mu Yuda ndi Yerusalemu! Zimene Yehova akunena kwa inu ndi izi: ‘Musaope kapena kutaya mtima chifukwa cha gulu lalikulu lankhondo ili. Pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu. 17 Sikudzafunika kuti Inu mumenyane nawo pa nkhondo imeneyi. Inu mukhale pa malo anu; imani molimba ndipo onani chipulumutso chimene Yehova adzakupatsani, Inu Yuda ndi Yerusalemu. Musaope, musataye mtima. Pitani kuti mukakumane nawo mawa, ndipo Yehova adzakhala nanu.’ "
22 Atangoyamba kuyimba ndi kutamanda, Yehova anapereka mʼmanja mwawo anthu a ku Amoni ndi a ku Mowabu ndiponso a ku Phiri la Seiri amene amalimbana ndi Yuda, ndipo anagonjetsedwa.