Pemphero la Hezekiya
14 Hezekiya analandira kalata kwa amithenga aja nayiwerenga. Pomwepo anapita ku Nyumba ya Yehova nayika kalatayo pamaso pa Yehova. 15 Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova nati, "Inu Yehova Mulungu wa Israeli, Inu amene mumakhala pa Akerubi, Inu nokha ndinu Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
19 Ndipo tsopano Inu Yehova Mulungu wathu, tipulumutseni ndithu mʼdzanja lake, kuti maufumu onse a dziko lapansi adziwe kuti Inu nokha, Inu Yehova, ndinu Mulungu."
35 Usiku umenewo mngelo wa Yehova anapita ku misasa ya ku Asiriya ndi kupha ankhondo 185,000. Ndipo pamene anthu anadzuka mmawa, taonani, mitembo inali ngundangunda!