5 Kotero Petro anasungidwa mʼndende, koma mpingo unamupempherera kolimba kwa Mulungu.
7 Mwadzidzidzi mngelo wa Ambuye anaonekera ndipo kuwala kunawunika mʼchipindamo. Mngeloyo anamugwedeza Petro mʼnthiti ndi kumudzutsa. Iye anati, "Fulumira, imirira!" Ndipo maunyolo anagwa kuchoka mʼmanja a Petro.
10 Iwo anadutsa gulu loyamba ndi lachiwiri la asilikali ndipo anafika pa chitseko chachitsulo cholowera mu mzinda. Chitsekocho chinatsekuka chokha ndipo anadutsa. Pamene anayenda kutalika kwa msewu umodzi, mwadzidzidzi mngelo uja anachoka.
12 Atazindikira zimenezi anapita ku nyumba ya Mariya amayi ake a Yohane, wotchedwanso Marko, kumene kunasonkhana anthu ambiri ndipo amapemphera. 13 Petro anagogoda pa chitseko cha panja, ndipo mtsikana wantchito dzina lake Roda anabwera kuti adzatsekule chitseko. 14 Atazindikira mawu a Petro anakondwa kwambiri ndipo anabwerera osatsekula ndipo anafuwula kuti, "Petro ali pa khomopa!"
15 Anthuwo anati kwa iye, "Wopenga iwe!" Atalimbikira kunena kuti zinali zoona, iwo anati, "Ameneyo ndi mngelo wake."
16 Koma Petro anapitiriza kugogoda ndipo atatsekula chitseko ndi kumuona, anthuwo anadabwa kwambiri.