Ku Korinto
1 Zitatha izi, Paulo anachoka ku Atene ndipo anapita ku Korinto. 2 Kumeneko anakumana ndi Myuda wina dzina lake Akula, nzika ya ku Ponto amene anali atangofika kumene kuchokera ku Italiya pamodzi ndi mkazi wake Prisila, chifukwa Klaudiyo analamula Ayuda onse kuti achoke ku Roma. Paulo anapita kukawaona. 3 Popeza Paulo anali mʼmisiri wosoka matenti monga iwo, iye anakhala nawo namagwirira ntchito pamodzi. 4 Tsiku la Sabata lililonse Paulo amakambirana ndi anthu mʼsunagoge, kufuna kukopa Ayuda ndi Agriki.
5 Sila ndi Timoteyo atafika kuchokera ku Makedoniya, Paulo ankangogwira ntchito yolalikira yokha basi, kuchitira umboni Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu. 6 Koma pamene Ayuda anatsutsana naye ndi kumuchita chipongwe, iye anakutumula zovala zake nati, "Magazi anu akhale pamitu yanu! Ine ndilibe mlandu. Kuyambira tsopano ndipita kwa anthu a mitundu ina."
7 Ndipo Paulo anatuluka mʼsunagoge napita ku nyumba yoyandikana ndi sunagoge ya Tito Yusto, munthu wopembedza Mulungu. 8 Krispo, mkulu wa sunagoge, pamodzi ndi a pa banja lake lonse anakhulupirira Ambuye; ndiponso Akorinto ambiri amene anamva Paulo akulalikira anakhulupiriranso nabatizidwa.
9 Usiku wina Ambuye anaonekera kwa Paulo mʼmasomphenya namuwuza kuti, "Usaope, pitiriza kuyankhula, usakhale chete. 10 Pakuti Ine ndili nawe, palibe aliyense amene adzakukhudza ndi kukuchitira choyipa, chifukwa mu mzinda muno ndili ndi anthu ambiri." 11 Choncho Paulo anakhala kumeneko chaka ndi miyezi isanu ndi umodzi akuphunzitsa Mawu a Mulungu.