12 Galiyo ali mkulu wa boma wa ku Akaya, Ayuda mogwirizana anamugwira Paulo napita naye ku bwalo la milandu. 13 Iwo anati, "Munthu uyu akukopa anthu kuti azipembedza Mulungu mwanjira zotsutsana ndi malamulo athu."
14 Pamene Paulo ankati ayankhule, Galiyo anati kwa Ayuda, "Ukanakhala mlandu wochita choyipa kapena wolakwira mnzake, bwenzi nditakumverani bwinobwino. 15 Koma popeza ndi nkhani yokhudza mawu, mayina ndi malamulo anu, kambiranani nokhanokha. Ine sindidzaweruza zinthu zimenezi." 16 Kotero iye anawapirikitsa mʼbwalo la milandu. 17 Kenaka iwo anagwira Sositene, mkulu wa sunagoge, ndipo anamumenya mʼbwalo la milandu momwemo. Koma Galiyo sanasamale zimenezi.