Pular para o conteúdo
Publicidade

Danieli 4:28-37

Maloto Akwaniritsidwa

28 Zonsezi zinamuchitikira mfumu Nebukadinezara. 29 Itapita miyezi khumi ndi iwiri, pamene mfumu inkayenda pa denga la nyumba ya ufumu ya ku Babuloni, 30 iye anati, "Kodi Babuloni si mzinda wamphamvu ndi wokongola umene ndinamanga ndi mphamvu zanga ngati nyumba yanga yaufumu, kuonetsera ulemerero wa ufumu wanga?"

31 Akuyankhulabe izi mawu anamveka kuchokera kumwamba kuti, "Imvani izi, mfumu Nebukadinezara: Ufumu wako wachotsedwa. 32 Udzachotsedwa pakati pa anthu ndipo udzakhala ndi zirombo zakuthengo; udzadya udzu monga ngʼombe. Zaka zisanu ndi ziwiri zidzadutsa mpaka iwe utavomereza kuti Wammwambamwamba ndiye mwini ulamuliro pa maufumu a anthu ndipo amawupereka kwa aliyense amene iye afuna."

33 Nthawi yomweyo zonse zimene zinanenedwa zokhudza Nebukadinezara zinakwaniritsidwa. Iye anachotsedwa pakati pa anthu ndipo ankadya udzu ngati ngʼombe. Thupi lake linanyowa ndi mame akumwamba mpaka tsitsi lake linakula ngati nthenga za chiwombankhanga ndi zikhadabo ngati zikhadabo za mbalame.

34 Pomaliza pa zaka zimenezo ine, Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndipo nzeru zanga zinabwereramo. Kenaka ndinatamanda Wammwambamwamba; ndinamupatsa ulemu ndi kumulemekeza Iye amene akhala nthawi zonse.

Ulamuliro wake ndi ulamuliro wa nthawi zonse;

ufumu wake udzakhala ku mibadomibado.

35 Anthu onse a dziko lapansi

ali chabe pamaso pake.

Pakati pa angelo akumwamba

ndi anthu a dziko lapansi

palibe amene akhoza kumuletsa

Mulungu kuchita zimene afuna.

Kapena kunena kwa Iye kuti, "Kodi mwachita chiyani?"

36 Pa nthawi yomweyo nzeru zanga zinabwereramo. Ndinalandiranso ulemu wanga ndi ufumu wanga. Nduna ndi akalonga anga anandilandiranso. Ndipo anandibwezera ufumu wanga ndi kukhalanso wamphamvu kuposa kale. 37 Tsopano ine Nebukadinezara, ndikutamanda, kukweza ndi kulemekeza Mfumu yakumwamba chifukwa zonse zimene amachita ndi zoyenera ndipo njira zake zonse ndi zachilungamo. Ndipo onse amene amayenda modzikuza adzawatsitsa.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.