Pular para o conteúdo
Publicidade

Danieli 9:4-19

4 Ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kuvomereza kuti tinachimwa:

Ndinati, "Inu Ambuye, Mulungu wamkulu ndi woopsa, amene mumasunga pangano lanu la chikondi kwa onse amene amakukondani ndi kumvera malamulo anu, 5 tachimwa ndipo tachita zolakwa ndi zoyipa. Takuwukirani posiya malangizo ndi malamulo anu. 6 Sitinamvere aneneri atumiki anu, amene anayankhula mʼdzina lanu kwa mafumu athu, kwa akalonga athu, makolo athu, ndi kwa anthu onse a mʼdziko.

7 "Ambuye ndinu olungama, koma lero tili ndi manyazi, ife anthu a ku Yuda, a ku Yerusalemu ndi Israeli yense, apafupi ndi akutali omwe, ku mayiko onse kumene munatipirikitsira chifukwa cha kusakhulupirika kwathu. 8 Inu Yehova, ife ndi mafumu athu, akalonga athu ndi makolo athu tili ndi manyazi chifukwa takuchimwirani. 9 Ambuye Mulungu wathu ndi wachifundo ndi wokhululuka, ngakhale kuti tamuwukira: 10 Ife sitinamvere Yehova Mulungu wathu kapena kusunga malamulo ake amene anatipatsa kudzera mwa aneneri atumiki ake. 11 Aisraeli onse anachimwira lamulo lanu motero anapatuka, nakana kukumverani.

"Choncho matemberero ndi olumbira amene alembedwa mʼmalamulo a Mose, mtumiki wa Mulungu, atigwera chifukwa takuchimwirani. 12 Inu mwakwaniritsa mawu amene munayankhula otitsutsa ife ndi otsutsa otilamulira potibweretsera tsoka lalikulu. Pa dziko lapansi sipanachitikenso zinthu ngati zimene zaonekera Yerusalemu. 13 Monga kunalembedwa mʼMalamulo a Mose, tsoka lililonse latifikira chikhalirecho sitinapemphe Yehova Mulungu wathu kuti atikomere mtima. Sitinasiye machimo athu, ndipo sitinasamale choonadi chanu. 14 Choncho Yehova anakonza kuti atigwetsere tsoka limeneli, ndipo wachitadi popeza Yehova Mulungu wathu ndi wolungama mu chilichonse amachita; chikhalirecho ife sitinamumvere.

15 "Inu Ambuye Mulungu wathu, munatulutsa anthu anu ku Igupto ndi dzanja lanu lamphamvu ndipo dzina lanu ndi lotchuka mpaka lero. Ife tachimwa, tachita zolakwa. 16 Inu Ambuye, molingana ndi zochita zanu zolungama, tikukupemphani kuti muchotse mkwiyo ndi ukali wanu pa Yerusalemu mzinda wanu, phiri lanu loyera. Machimo athu ndi mphulupulu za makolo athu zachititsa kuti onse otizungulira atonze Yerusalemu ndi anthu anu.

17 "Tsopano Mulungu wathu, imvani mapemphero ndi zopempha za mtumiki wanu. Kuti anthu onse akudziweni kuti ndinu Ambuye, komerani mtima malo anu opatulika amene asanduka bwinja. 18 Tcherani khutu, Inu Mulungu, ndipo imvani; tsekulani maso anu ndipo onani mabwinja athu ndi mzinda umene umadziwika ndi dzina lanu. Sitikupempha chifukwa chakuti ndife olungama, koma chifukwa cha kukula kwa chifundo chanu. 19 Inu Ambuye imvani mawu athu! Ambuye khululukani! Ambuye timvereni, ndipo muchitepo kanthu! Kuti anthu adziwe kuti Inu ndinu Mulungu wanga musachedwe chifukwa mzinda wanu ndi anthu anu amadziwika ndi dzina lanu."

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.