Pular para o conteúdo
Publicidade

Deuteronomo 14:22,23,26,28,29

Za Chakhumi

22 Muzionetsetsa kuti mukupatula chakhumi pa zokolola zanu chaka chilichonse. 23 Muzidyera chakhumi cha tirigu wanu, vinyo wanu watsopano ndi mafuta, ndi ana oyamba kubadwa a ngʼombe zanu pamaso pa Yehova Mulungu wanu pa malo amene adzasankhe ngati kokhalako dzina lake, kuti muphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu. 26 Gwiritsani ntchito silivayo kugula chilichonse chimene muchifuna monga ngʼombe, nkhosa, vinyo kapena zakumwa zina zosasitsa, kapena china chilichonse chimene muchifuna. Ndipo inu ndi anthu a pa banja panu mudzazidyera komweko pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi kukondwera.

28 Kumapeto kwa zaka zitatu zilizonse muzibweretsa zakhumi zonse pa zokolola za chaka chimenecho ndi kuzisunga mʼmidzi yanu, 29 kuti Alevi (amene alibe gawo lawo la chuma kapena cholowa chawochawo), alendo, ana ndi akazi amasiye, amene akukhala mʼmizinda yanu akhoza kubwera kudzadya ndi kukhuta. Ndipo kuti akutero Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa ntchito zanu zonse.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.