Pular para o conteúdo
Publicidade

Deuteronomo 8:11-14,17,18

11 Samalani kuopa kuti mungayiwale Yehova Mulungu wanu posasunga malamulo, zikhazikitso ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, 12 kuopa kuti mukadya ndi kukhuta, mukamanga nyumba zabwino ndi kukhalamo, 13 ndi pamene ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu zaswana, ndi siliva ndi golide wanu wachuluka ndiponso kuti zonse zimene muli nazo zachuluka, 14 mtima wanu udzayamba kunyada ndi kuyiwala Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto, kukuchotsani ku dziko la ukapolo. 17 Mu mtima mwanu mukhoza kuganiza kuti, "Mphamvu zanga ndi kulimbika kwa dzanja langa ndi zimene zandilemeretsa chonchi." 18 Koma kumbukirani Yehova Mulungu chifukwa ndi amene amakupatsani mphamvu zopezera chuma chimenechi kuti atsimikize pangano limene analumbira kwa makolo anu, monga liliri lero lino.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.