Pular para o conteúdo
Publicidade

Aefeso 4:1-12

Umodzi Mʼthupi la Khristu

1 Ine monga wamʼndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukulimbikitsani kuti mukhale moyo woyenera mayitanidwe amene munalandira. 2 Mukhale odzichepetsa kwathunthu ndi ofatsa; mukhale oleza mtima, ololerana wina ndi mnzake mwachikondi. 3 Muyesetse kusunga umodzi wa Mzimu; umodzi umene umatimangirira pamodzi mu mtendere. 4 Pali thupi limodzi ndiponso Mzimu mmodzi, monganso pali chiyembekezo chimodzi chimene anakuyitanirani. 5 Pali Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi; 6 Mulungu mmodzi ndi Atate a onse, ndipo ali mwa onse.

7 Koma aliyense wa ife wapatsidwa chisomo molingana ndi muyeso wa mphatso ya Khristu. 8 Nʼchifukwa chake akunena kuti,

"Iye atakwera kumwamba,

anatenga chigulu cha a mʼndende

ndipo anapereka mphatso kwa anthu."

9 Kodi mawu akuti, "Iye anakwera" akutanthauza chiyani, ngati Iyeyo sanatsikire kunsi kwa dziko lapansi? 10 Iye amene anatsika ndi yemweyo anakwera koposa mʼmayiko a kumwamba onse, ndi cholinga choti zinthu zonse zikhale zodzaza ndi Iye. 11 Iye ndiye amene anapereka mphatso kwa ena kuti akhale atumwi ndi ena aneneri, ena alaliki, ndi ena abusa ndi aphunzitsi. 12 Ntchito yawo ndi kukonza oyera mtima kuti agwire ntchito ya utumiki kuti thupi la Khristu lilimbikitsidwe.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.