Pular para o conteúdo
Publicidade

Eksodo 17:1-7

Madzi Otuluka Mʼthanthwe

1 Gulu lonse la Aisraeli linachoka ku chipululu cha Sini, ndi kumayenda malo ndi malo monga momwe anawalamulira Yehova. Iwo anamanga misasa yawo ku Refidimu koma kunalibe madzi woti anthu onse ndi kumwa. 2 Kotero iwo anakangana ndi Mose nati, "Tipatse madzi akumwa."

Mose anayankha kuti, "Chifukwa chiyani mukukangana ndi ine? Chifukwa chiyani mukumuyesa Yehova?"

3 Koma anthu anali ndi ludzu pamenepo ndipo anangʼungʼudza pamaso pa Mose namufunsa kuti, "Kodi nʼchifukwa chiyani unatitulutsa mʼdziko la Igupto kuti ife, ana athu pamodzi ndi ziweto zathu tife ndi ludzu?"

4 Ndipo Mose anapemphera kwa Yehova, "Kodi ndichite chiyani ndi anthu awa? Iwo atsala pangʼono kundigenda ndi miyala."

5 Yehova anati kwa Mose, "Pita patsogolo pa anthuwo. Tenga ndodo imene unamenyera nyanja ya Nailo pamodzi ndi akuluakulu ena a Israeli ndi kunyamuka. 6 Ine ndidzayima patsogolo pako pafupi ndi thanthwe la ku Horebu. Ukamenye thanthwelo, madzi adzatuluka kuti anthu amwe." Motero Mose anachita zimenezi pamaso pa akuluakulu a Israeli. 7 Ndipo iye anatcha malowo Masa ndi Meriba chifukwa Aisraeli anakangana ndi kuyesa Yehova ponena kuti, "Kodi pakati pathu pali Yehova kapena palibe?"

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.