Chihema cha Mapemphero
1 "Panga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso apete pa nsaluzo Akerubi.
7 "Upange nsalu za ubweya wambuzi zophimba pamwamba pa chihemacho. Nsalu zonse pamodzi zikhale khumi ndi imodzi. 14 Upange chikopa cha nkhosa zazimuna cha utoto wofiira chophimbira tentiyo ndipo pamwamba pake upangireponso chophimbira china cha zikopa za akatumbu.
15 "Upange maferemu amatabwa amtengo wa mkesha oyimikira chihemacho.
31 "Upange nsalu yokhala ndi mtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira ndipo nsaluyo ikhale yolukidwa bwino, yofewa ndi yosalala. Ndipo anthu aluso apetepo zithunzi za Akerubi. 33 Ukoloweke kataniyo ku ngowe ndipo uyike Bokosi la Chipangano mʼkatimo. Kataniyo idzalekanitse malo wopatulika ndi malo wopatulika kwambiri.