Za Beseni Losambira
17 Ndipo Yehova anati kwa Mose, 18 "Upange beseni lamkuwa lokhala ndi miyendo yamkuwanso. Uliyike pakati pa tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe ndipo uthiremo madzi. 19 Aaroni ndi ana ake azisamba mʼmanja ndi kutsuka mapazi awo ndi madzi amenewo. 20 Pamene akulowa mu tenti ya msonkhano, iwo asambe madziwa kuti asafe. Ndiponso pamene akupita kukatumikira ku guwa lansembe ndi kupereka nsembe yopsereza kwa Yehova, 21 azisamba mʼmanja mwawo ndi kutsuka mapazi kuti asadzafe. Limeneli ndi lamulo limene Aaroni, pamodzi ndi ana ndi zidzukulu zake mʼtsogolomo ayenera kumadzalitsatira mpaka muyaya."