21 ndipo aliyense amene anakhudzidwa mu mtima mwake nafuna kupereka, anabwera kudzapereka chopereka kwa Yehova cha ntchito yokonza tenti ya msonkhano, cha ntchito zonse za mʼtentimo ndi cha zovala zopatulika. 22 Onse amene anali ndi mtima wofuna, amuna ndi amayi omwe anabwera kudzapereka zodzikometsera zagolide za mtundu uliwonse: zomangira zovala, ndolo, mphete ndi zokometsera. Onse anapereka golide wawo monga nsembe yoweyula pamaso pa Yehova. 29 Aisraeli onse aamuna ndi aakazi amene anali ndi mtima wofuna, anabweretsa kwa Yehova chopereka chaufulu ku ntchito yonse ya Yehova imene analamulira kudzera mwa Mose kuti achite.
Publicidade