Pular para o conteúdo
Publicidade

Genesis 14:14-16,18-20

14 Abramu atamva kuti Loti wagwidwa pa nkhondo, anasonkhanitsa asilikali 318 obadwira mʼbanja lake lomwelo nalondola mpaka ku Dani. 15 Pa nthawi ya usiku Abramu anawagawa asilikali ake kuti athire nkhondo mafumu aja, ndipo anawakantha nawapirikitsa mpaka ku Hoba, cha kumpoto kwa Damasiko. 16 Ndipo anawalanda katundu wawo yense nabwera naye Loti, katundu wake yense, pamodzi ndi akazi ndi anthu ena.

18 Ndipo Melikizedeki mfumu ya ku Salemu anabweretsa buledi ndi vinyo. Iyeyu anali wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba, 19 ndipo anadalitsa Abramu nati,

"Mulungu Wammwambamwamba,

wolenga kumwamba ndi dziko lapansi, akudalitse iwe Abramu.

20 Ndipo adalitsike Mulungu Wammwambamwamba

amene anapereka adani ako mʼdzanja lako."

Ndipo Abramu anamupatsa iye chakhumi cha zonse anali nazo.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.