Kuyesedwa kwa Abrahamu
1 Nthawi ina zitatha izi, Mulungu anamuyesa Abrahamu. Iye anati, "Abrahamu!"
Ndipo iye anayankha kuti, "Ee Ambuye."
2 Ndipo Mulungu anati, "Tenga Isake, mwana wako yekhayo amene umamukonda ndi kupita naye ku dziko la Moriya. Ukamupereke iye ngati nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri a kumeneko limene ndidzakuwuza."
12 Mngeloyo anati, "Usatambasulire mwanayo dzanja lako kuti umuphe, pakuti tsopano ndadziwa kuti iwe umaopa Mulungu. Iwe sunandimane mwana wako mmodzi yekhayo."