3 Patapita nthawi, Kaini anatenga zipatso za ku munda nakazipereka kwa Yehova monga nsembe. 4 Nayenso Abele anatenga ana ankhosa oyamba kubadwa pamodzi ndi mafuta ake nakazipereka ngati nsembe kwa Yehova. Yehova anakondwera ndi Abele ndi nsembe yake. 5 Koma sanakondwere ndi Kaini ndi nsembe yake. Kotero Kaini anakwiya kwambiri ndipo nkhope yake inagwa.
6 Choncho Yehova anati kwa Kaini, "Chifukwa chiyani wakwiya ndipo bwanji nkhope yako yagwa? 7 Ukanachita zabwino sindikanakulandira kodi? Koma tsopano wachita zoyipa ndipo tchimo likukudikira pa khomo pako, likufuna kukugwira; koma iwe uyenera kugonjetsa tchimolo."