Pular para o conteúdo
Publicidade

Ahebri 10:3-10

3 Koma nsembezo zimawakumbutsa anthuwo machimo awo chaka ndi chaka. 4 Chifukwa nʼkosatheka kuti magazi angʼombe yayimuna ndi mbuzi yayimuna achotse machimo.

5 Nʼchifukwa chake Khristu atabwera pa dziko lapansi anati,

"Simunafune nsembe kapena zopereka,

koma thupi munandikonzera.

6 Simunakondwere nazo nsembe zopsereza

ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo.

7 Tsono, Ine ndinati, ‘Ndili pano Ine,

Inu Mulungu, ndabwera kudzachita zimene mukufuna monga zinalembedwa mʼMalemba.’ "

8 Poyamba Iye anati, "Nsembe kapena zopereka zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo, Inu simunazifune kapena kukondwera nazo." Ngakhale kuti Malamulo ndiye amanena kuti ziperekedwe. 9 Pamenepo Iye anati, "Ndili pano Ine, ndabwera kudzachita zimene mukufuna." Khristu anachotsa nsembe zoyamba zija kuti mʼmalo mwake ayikemo nsembe za mtundu wachiwiri. 10 Chifukwa chakuti Yesu Khristu anachita zimene Mulungu anafuna kuti achite, ndife oyeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene analipereka kamodzi kokha.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.