Pular para o conteúdo
Publicidade

Ahebri 3:7,8,12,13,15

Chenjezo pa Kusakhulupirira

7 Tsono monga Mzimu Woyera akuti,

"Lero mukamva mawu ake,

8 musawumitse mitima yanu

ngati munachitira pamene munawukira,

pa nthawi yoyesedwa mʼchipululu.

12 Abale samalani, kuti pasapezeke wina aliyense mwa inu wokhala ndi mtima woyipa ndi wosakhulupirira, womulekanitsa ndi Mulungu wamoyo. 13 Koma muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku, ikanalipo nthawi imene imatchedwa kuti "Lero" kuti aliyense wa inu mtima wake usawumitsidwe ndi chinyengo cha tchimo. 15 Monga kunanenedwa kuti,

"Lero ngati mumva mawu ake,

musawumitse mitima yanu

ngati momwe munachitira pamene munawukira."

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.