Yesu Mkulu wa Ansembe Wopambana
14 Popeza kuti tili ndi Mkulu wa ansembe wopambana, amene analowa kale kumwamba, Yesu Mwana wa Mulungu, tiyeni tigwiritsitse chikhulupiriro chathu chimene timavomereza. 15 Pakuti sitili ndi Mkulu wa ansembe amene sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofowoka zathu. Koma tili naye amene anayesedwa mʼnjira zonse monga ife, koma sanachimwe.