Pular para o conteúdo
Publicidade

Yohane 19:12-16

TCCL Abra a Palavra de Deus em Chichewa Contemporâneo

12 Kuyambira pamenepo Pilato anayesa kuti amumasule Yesu, koma Ayuda anapitirira kufuwula kuti, "Ngati mumumasula munthuyu kuti apite, inu si bwenzi la Kaisara."

13 Pilato atamva zimenezi, iye anamutulutsa Yesu kunja ndi kukhala pansi pa mpando wa woweruza pamalo otchedwa Mwala Wowaka (umene pa Chiaramaiki ndi Gabata). 14 Linali tsiku lokonzekera Sabata la Paska ndipo nthawi inali ora lachisanu ndi chimodzi masana.

Pilato anati kwa Ayuda, "Nayi mfumu yanu."

15 Koma iwo anafuwula kuti, "Choka nayeni! Choka nayeni! Mpachikeni!"

Pilato anafunsa kuti, "Kodi ine ndipachike mfumu yanuyi?"

Akulu a ansembe anayankha kuti, "Ife tilibe mfumu ina koma Kaisara."

16 Pomaliza Pilato anamupereka kwa iwo kuti akapachikidwe. Choncho asilikali anamutenga Yesu.

Em outras traduções

  1. NTNYBL2025 Nyanja

    12 Kuyambila pamenepo Pilato wamafuna njila ya kumsiilila, nambho Ayahudi adakweza mvekelo adakamba, "Ukamsiilila uyu, iwe asati bwenji lake Kaisali, waliyonjhe uyo wajhichita mfumu wamchucha Kaisali!"

    13 Ndiipo Pilato yapo waadavela mawu yameneyo wadamtulucha Yesu kubwalo, wadakhala pampando wa ulamuli pamalo yapo patanidwa "Gabata" Mate yake sakafu ya Myala.

    14 Idali ngati sasita za usana, siku yokonjekela Pasaka. Pilato wadaakambila Ayahudi, "Mfumu wanu yuno pano!"

    15 Adakweza mvekelo, "Mchoche! Mchoche!"

    Pilato wadafunjha, "Nimpachike pamtanda Mfumu wanu?"

    Ajhukulu waakulu adayangha, "Ife tilibe Mfumu mwina nambho Kaisali pe!"

    16 Chimwecho, Pilato wadaapacha Yesu kuti ampachike achinawene.

    Ndiipo, adamtenga Yesu.

Direitos das traduções citadas

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.