Pular para o conteúdo
Publicidade

Yohane 19:17-19,23-30

Kupachikidwa kwa Yesu

17 Atanyamula mtanda wake, anapita kumalo otchedwa "Malo a Bade" (mʼChiaramaiki amatchedwa Gologota). 18 Pamenepo iwo anamupachika Iye pamodzi ndi anthu ena awiri, mmodzi mbali ina ndi wina mbali inanso ndipo Yesu pakati.

19 Pilato analemba chikwangwani chomwe anachikhoma pa mtandapo. Panalembedwa mawu akuti, yesu wa ku nazareti, mfumu ya ayuda.

23 Asilikali atamupachika Yesu, anatenga zovala zake ndi kuzigawa zigawo zinayi, gawo limodzi la aliyense wa iwo, ndi kutsala mwinjiro wamʼkati wokha. Chovala ichi chinawombedwa kuyambira pamwamba mpaka pansi wopanda msoko.

24 Iwo anati kwa wina ndi mnzake, "Tiyeni tisachingʼambe koma tichite maere kuti tione amene achitenge."

Izi zinachitika kuti malemba akwaniritsidwe amene anati,

"Iwo anagawana zovala zanga pakati pawo

ndi kuchita maere pa zovala zangazo."

Choncho izi ndi zimene asilikali anachita.

25 Pafupi ndi mtanda wa Yesu panayima amayi ake, mngʼono wa amayi ake, Mariya mkazi wa Kaliyopa ndi Mariya wa ku Magadala. 26 Yesu ataona amayi ake pamenepo ndi wophunzira amene Iye anamukonda atayima pafupipo, Iye anati kwa amayi ake, "Amayi nayu mwana wanu." 27 Anawuzanso wophunzirayo kuti, "Nawa amayi ako." Kuyambira nthawi imeneyo, wophunzirayo anatenga amayiwo kupita nawo kwawo.

Imfa ya Yesu

28 Atadziwa kuti zonse zatha tsopano komanso kuti malemba akwaniritsidwe, Yesu anati, "Ine ndili ndi ludzu." 29 Pomwepo panali mtsuko wodzaza ndi vinyo wosasa, choncho iwo ananyika chinkhupule ndi kuchisomeka ku mtengo wa hisope nachifikitsa kukamwa kwa Yesu. 30 Yesu atalandira chakumwachi anati, "Kwatha." Ndipo Iye anaweramitsa mutu wake napereka mzimu wake.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.