36 Gideoni anati kwa Mulungu, "Ngati mudzapulumutsa Israeli ndi dzanja langa monga mwalonjezeramu, 37 onani, ine ndiyala ubweya wankhosa pa malo opunthira tirigu. Ngati mame adzagwera pa ubweya wankhosa pokhapa, pa nthaka ponse pakhala powuma, ndiye ndidziwa kuti mudzapulumutsadi Israeli ndi dzanja langa monga mwanenera." 38 Ndipo zimenezi zinachitikadi. Gideoni atadzuka mʼmamawa ndi kuwufinya ubweya uja, anafinya madzi odzaza mtsuko.
39 Kenaka Gideoni anati kwa Mulungu, "Musandikwiyire. Mundilole ndiyankhule kamodzi kokhaka. Ndiyeseko kamodzi kokha ndi ubweyawu kuti pa ubweya pokhapa pakhale powuma koma pa nthaka ponse pakhale ponyowa ndi mame." 40 Ndipo Mulungu anachita zomwezo usiku umenewo. Pa ubweya pokha panali powuma, koma pa nthaka ponse panagwa mame.