Pular para o conteúdo
Publicidade

Luka 11:1-13

Yesu Aphunzitsa za ku Pemphera

1 Tsiku lina Yesu amapemphera pamalo ena. Atamaliza, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, "Ambuye tiphunzitseni kupemphera, monga momwe Yohane anaphunzitsira ophunzira ake."

2 Yesu anawawuza kuti, "Pamene mukupemphera muzinena kuti:

" ‘Atate,

dzina lanu lilemekezedwe,

ufumu wanu ubwere.

3 Mutipatse chakudya chathu chalero,

4 mutikhululukire machimo athu,

monga ifenso timakhululukira aliyense amene watilakwira.

Ndipo musalole kuti tigwe mʼmayesero.’ "

5 Kenaka anawawuza kuti, "Tiyerekeze: Mmodzi mwa inu atakhala ndi bwenzi lake, ndipo iye nʼkupita ku nyumba yake pakati pa usiku, nakanena kuti, ‘Mnzanga, bwereke malofu atatu abuledi, 6 chifukwa ndalandira bwenzi langa amene ali pa ulendo ndipo ine ndilibe choti ndimupatse.’

7 "Ndipo yerekezani kuti amene ali mʼnyumbamo ndi kuyankha kuti, ‘Usandivutitse ine, ndatseka kale chitseko, ndipo ine ndi ana anga tagona. Ine sindingadzukenso kuti ndidzakupatse.’ 8 Ine ndikukuwuzani kuti adzadzuka ndi kumupatsa bulediyo, osati chifukwa ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha liwuma la munthu wopemphayo, ndipo kudzamupatsa zonse zimene akuzifuna.

9 "Choncho Ine ndikunena kwa inu kuti: Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza. Gogodani ndipo adzakutsekulirani. 10 Pakuti aliyense amene amapempha amalandira. Munthu amene amafunafuna amapeza. Iye amene amagogoda amamutsekulira.

11 "Ndani mwa inu abambo, kodi mwana wanu atapempha nsomba, mʼmalo mwake mungamupatse njoka? 12 Kapena atapempha dzira, kodi mungamupatse chinkhanira? 13 Tsono ngati inu, anthu oyipa, mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, koposa kotani Atate anu akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene awapempha!"

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.