Pular para o conteúdo
Publicidade

Luka 15:12-14,16-18,20

12 Wamngʼonoyo anati kwa abambo ake, ‘Abambo, patseni gawo langa la chuma chanu.’ Ndipo iye anawagawira awiriwo chuma chawo.

13 "Pasanapite nthawi, wamngʼonoyo anasonkhanitsa chuma chake chonse, napita ku dziko lakutali ndipo kumeneko anayamba kumwaza chuma chake mʼnjira zachitayiko. 14 Iye atawononga zonse, kunagwa njala yoopsa mʼdziko lonselo ndipo anayamba kusauka. 16 Iye analakalaka atakhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumbazo zinkadya, koma panalibe wina amene anamupatsa kanthu.

17 "Maganizo ake atabweramo, iye anati, ‘Ndi antchito angati a abambo anga amene ali ndi chakudya chimene amadya nʼkutsalako ndipo ine ndili pano kufa ndi njala! 18 Ine ndinyamuka ndi kubwerera kwa abambo anga ndipo ndikati kwa iwo: abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi kwa inu. 20 Ndipo iye ananyamuka ndi kupita kwa abambo ake.

"Koma iye akanali patali, abambo ake anamuona ndipo anamvera chisoni; anathamangira mwanayo, namukumbatira ndi kupsompsona.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.