Munthu Wachuma ndi Ufumu wa Mulungu
18 Oweruza wina wake anamufunsa Iye kuti, "Aphunzitsi abwino, ndichite chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?"
22 Yesu atamva izi, anati kwa iye, "Ukusowabe chinthu chimodzi: Gulitsa zonse zimene uli nazo ndipo uzipereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Kenaka ubwere, nunditsate ine."
23 Atamva zimenezi, anakhumudwa kwambiri chifukwa anali munthu wachuma chambiri. 24 Yesu anamuyangʼana nati, "Nʼkwapatali kwambiri kuti anthu achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu! 25 Ndithudi, nʼkwapafupi kuti ngamira idutse pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kulowa mu ufumu wa Mulungu."
26 Amene anamva izi anafunsa kuti, "Nanga ndani amene angapulumuke?"
27 Yesu anayankha kuti, "Zinthu zosatheka ndi anthu zimatheka ndi Mulungu."