Pular para o conteúdo
Publicidade

Levitiko 6:1-5

1 Yehova anawuza Mose kuti, 2 "Ngati munthu wina aliyense achimwa, nachita zinthu mosakhulupirika kwa Yehova chifukwa cha kunyenga mnzake pokana kumubwezera zimene anamusungitsa, kapena kumubera kapenanso kumulanda, 3 kapena ndi kunama kuti sanatole chinthu chimene chinatayika, kapena kulumbira mwachinyengo pa chinthu chilichonse chimene munthu akachita amachimwa nacho, 4 ndi wopalamula ndithu, ndipo ayenera kubweza zimene anabazo, zimene analanda mwachinyengozo, zimene anamusungitsazo, zimene anatolazo 5 kapena zimene analumbira monyengazo. Pa tsiku limene apezeke kuti wapalamuladi, iye ayenera kumubwezera mwini wake zinthu zonsezi ndi kuwonjezerapo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.