17 Munthu wina mʼgululo anayankha kuti, "Aphunzitsi, ndinakubweretserani mwana wanga wamwamuna, amene ndi ogwidwa ndi mzimu umene umamulepheretsa kuyankhula.
22 wakhala ukumuponya pa moto kapena mʼmadzi kuti umuphe. Koma ngati mungathe kuchita kanthu, tichitireni chifundo ndipo mutithandize."
23 Yesu anati, " ‘Ngati mungathe!’ Zinthu zonse ndi zotheka kwa iye amene akhulupirira."
24 Nthawi yomweyo abambo a mwanayo anafuwula kuti, "Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga!"