7 Kuyambira nthawi ya makolo anu mwakhala mukuphwanya malamulo anga ndipo simunawatsatire. Bwererani kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu," akutero Yehova Wamphamvuzonse.
"Koma inu mukufunsa kuti, ‘Tibwerere motani kwa Yehova?’
8 "Kodi munthu angathe kuba za Mulungu? Komatu inu mumandibera.
"Koma inu mukufunsa kuti, ‘Kodi timakuberani motani?’
"Pa zakhumi ndi pa zopereka. 9 Mtundu wanu wonse ndinu otembereredwa, chifukwa mukundibera. 10 Bweretsani chakhumi chathunthu ku nyumba yosungira, kuti mukhale chakudya mʼnyumba mwanga." Akutero Yehova Wamphamvuzonse, "Tandiyesani, ndipo muone ngati sindidzatsekula zipata zakumwamba, ndi kukugwetserani madalitso ochuluka amene mudzasowe malo owayikamo. 11 Ndidzaletsa tizirombo kuti tisawononge mbewu zanu, ndipo mpesa wa mʼminda mwanu zipatso zake sizidzayoyoka," akutero Yehova Wamphamvuzonse.