Pular para o conteúdo
Publicidade

Mateyu 16:21-26

TCCL Abra a Palavra de Deus em Chichewa Contemporâneo

Yesu Aneneratu za Imfa Yake

21 Kuyambira nthawi imeneyo Yesu anayamba kuwafotokozera ophunzira ake kuti Iye ayenera kupita ku Yerusalemu ndi kukazunzidwa kwambiri mʼmanja mwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo kuti ayenera kuphedwa, ndi kuti tsiku lachitatu adzaukitsidwa.

22 Petro anamutengera Iye pambali nayamba kumudzudzula kuti, "Dzichitireni chifundo Ambuye, sizingachitike kwa Inu ayi."

23 Yesu anatembenuka nati kwa Petro, "Choka pamaso panga Satana! Iwe ndi chokhumudwitsa kwa Ine; iwe suganizira zinthu za Mulungu koma zinthu za anthu."

Za Kusenza Mtanda

24 Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, "Ngati wina aliyense abwera pambuyo panga ayenera kudzikana ndi kutenga mtanda wake ndi kunditsata Ine. 25 Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupeza. 26 Kodi munthu adzapindula chiyani ngati atapeza zonse za dziko lapansi nataya moyo wake? Kapena munthu angapereke chiyani chosinthana ndi moyo wake?

Em outras traduções

  1. NTNYBL2025 Nyanja

    21 Kuyambila nyengo imeneyo Yesu wadayamba kuwakambila padanga oyaluzidwa wake, "Nifunika nipite kumujhi wa Yelusalemu, ni kumeneko sinivutichidwe kupunda kupitila mmanja ya waakulu ni akuluakulu wa ajhukulu, ni oyaluza a thauko, ni kumeneko siniphedwe, ni siku la katatu sinihyuke."

    22 Pamenepo Petulo wadamtenga Yesu pambhepete, wadayamba kumnyindila, "Osati Ambuye, yaya siyadakupatani!" 23 Yesu wadamng’anamukila Petulo ni kumkambila, "Choka pamaso panga, Satana! Iwe ni chochelekeza kwanga. Ndande maganizo yako siyachoka kwa Mnungu, nambho ni maganizo ya wandhu!"

    24 Ndiipo Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake, "Mundhu uyo wafuna kunichata, poyamba wafunika wajhikane mwenewake ni kuutenga mtanda wake, wanichate. 25 Pakuti, mundhu uyo wafuna kuulamicha umoyo wake, siwautaize, ni mundhu uyo siwautaize umoyo wake ndande ya ine, siwaupate. 26 Pakuti, mundhu siwapate phindu lanji wakayapata yonjhe yali pajhiko, nambho wautaize umoyo wake? Kapina mundhu siwachoche chiyani kuti waupate umoyo wake?

Direitos das traduções citadas

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.