Yesu Adzudzula Aphunzitsi Amalamulo ndi Afarisi
1 Pamenepo Yesu anati kwa magulu a anthu ndi ophunzira ake: 2 "Aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi amakhala pa mpando wa Mose. 3 Choncho muziwamvera ndi kuchita chilichonse chimene akuwuzani. Koma musachite zimene amachita, popeza sachita zimene amaphunzitsa. 4 Amamanga akatundu olemera nawayika pa mapewa a anthu, koma iwo eni safuna kuwanyamula.
5 "Ntchito zawo amachita ndi cholinga chakuti anthu awaone. Amadzimangirira timaphukusi tikulutikulu ta Mawu a Mulungu pa mphumi ndi pa mkono komanso amatalikitsa mphonje za mikanjo yawo. 6 Amakonda malo aulemu pa maphwando ndi malo ofunika kwambiri mʼmasunagoge. 7 Amakondwera ndi kupatsidwa moni mʼmisika ndi kutchulidwa kuti ‘Aphunzitsi.’