Pular para o conteúdo
Publicidade

Mateyu 6:1-6,16-18

Zopereka Zachifundo

1 "Samalani kuti musachite ntchito zanu zolungama pamaso pa anthu kuti akuoneni. Popeza ngati mutero simudzalandira mphotho yochokera kwa Atate anu akumwamba.

2 "Pamene mupereka zachifundo, musachite modzionetsera monga amachita achiphamaso mʼmasunagoge ndi pa misewu kuti atamidwe ndi anthu. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwowo alandiriratu mphotho yawo yonse. 3 Koma pamene mupereka zachifundo, dzanja lanu lamanzere lisadziwe chimene dzanja lanu lamanja likuchita, 4 kotero kuti kupereka kwanu kukhale mwachinsinsi. Ndipo Atate anu amene amaona zochitika mwachinsinsi, adzakupatsani mphotho.

Za Kupemphera

5 "Pamene mupemphera, musakhale ngati achiphamaso, chifukwa iwo amakonda kupemphera choyimirira mʼmasunagoge ndi pa mphambano za mʼmisewu kuti anthu awaone. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse. 6 Koma pamene mupemphera, lowani mʼchipinda chanu chamʼkati, ndi kutseka chitseko ndipo mupemphere kwa Atate anu amene saoneka. Ndipo Atate anu, amene amaona zochitika mseri, adzakupatsani mphotho.

Kusala Kudya

16 "Pamene mukusala kudya, musaonetse nkhope yachisoni monga achita achiphamaso, pakuti iwo amasintha nkhope zawo kuonetsa anthu kuti akusala kudya. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse. 17 Koma pamene ukusala kudya, samba mʼmaso nudzole mafuta kumutu, 18 kuti usaonekere kwa anthu kuti ukusala kudya koma kwa Atate ako ali mseri; ndipo Atate ako amene amaona za mseri adzakupatsa mphotho.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.