Pemphani, Funafunani, Gogodani
7 "Pemphani ndipo mudzapatsidwa; funafunani ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsekulirani. 8 Pakuti wopempha aliyense amalandira; ndi wofuna amapeza; ndipo iye amene agogoda, adzamutsekulira.
9 "Ndani mwa inu, mwana wake akamupempha buledi amamupatsa mwala? 10 Kapena ngati mwana apempha nsomba, kodi amamupatsa njoka? 11 Tsono ngati inu woyipitsitsa mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanga Atate anu akumwamba sadzapereka mphatso zabwino kwa iwo amene amupempha?