Pular para o conteúdo
Publicidade

Mateyu 9:9-13

TCCL Abra a Palavra de Deus em Chichewa Contemporâneo

Kuyitanidwa kwa Mateyu

9 Ndipo Yesu atachoka kumeneko, anaona munthu wina dzina lake Mateyu, atakhala mʼnyumba ya msonkho. Anati kwa iye, "Nditsate Ine." Ndipo iye ananyamuka namutsata.

10 Ndipo pamene Iye ankadya mʼnyumba, onani, amisonkho ndi ochimwa ambiri anabwera nakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake. 11 Ndipo Afarisi poona izi, anati kwa ophunzira ake, "Nʼchifukwa chiyani Aphunzitsi anu akudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?"

12 Yesu atamva, anati, "Munthu wamoyo safuna singʼanga ayi, koma wodwala. 13 Koma pitani kaphunzireni tanthauzo la mawu awa: ‘Ndimafuna chifundo osati nsembe ayi.’ Pakuti sindinabwere kudzayitana olungama koma ochimwa."

Em outras traduções

  1. NTNYBL2025 Nyanja

    9 Yesu wadachokapo pamenepo, ni yapo wamachoka wadamuona mundhu mwina wolandila malipilo uyo watanidwa Matayo, wakhala mnyumba ya malipilo. Yesu wadamtana ni kumkambila, "Nichate."

    Matayo wadaima ni kumchata.

    10 Yesu yapo wamadya chakudya mnyumba ya Matayo, olandila malipilo ambili ni amachimo adajha kudya chakudya pamojhi ni Yesu ni oyaluzidwa wake. 11 Afalisayo yapoadaona yameneyo, wadaafunjha oyaluzidwa a Yesu, "Ndande yanjhi oyaluza wanu wakudya pamojhi ni olandila malipilo ni amachimo?"

    12 Yesu yapo wadavela yameneyo, wadakamba, "Wandhu yawo asangalala siafuna singanga nambho odwala. 13 Nambho mpite mkajhiyaluze mate ya mawu yaya, Nifuna lisungu, osati njhembe. Sinidajhe kwatana wandhu abwino nambho amachimo."

Direitos das traduções citadas

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.