Pular para o conteúdo
Publicidade

Numeri 14:1-9

Anthu Awukira

1 Usiku umenewo gulu lonse la Aisraeli linalira mofuwula kwambiri. 2 Ndipo Aisraeli onse anayankhula motsutsana ndi Mose ndi Aaroni. Gulu lonse linanena kwa iwo kuti, "Kunali bwino tikanafera ku Igupto kapena mʼchipululu muno! 3 Nʼchifukwa chiyani Yehova akutilowetsa mʼdziko limenelo? Kodi kuti tikaphedwe ndi lupanga? Kuti akazi ndi ana athu akatengedwe ngati katundu wolanda ku nkhondo? Kodi sikungakhale bwino kuti tibwerere ku Igupto?" 4 Ndipo anawuzana wina ndi mnzake kuti, "Tiyeni tisankhe mtsogoleri ndipo tibwerere ku Igupto."

5 Koma Mose ndi Aaroni anadzigwetsa pansi chafufumimba pamaso pa Aisraeli onse omwe anasonkhana pamenepo. 6 Yoswa mwana wa Nuni ndi Kalebe mwana wa Yefune, omwe anali amodzi mwa amene anakazonda nawo dziko, anangʼamba zovala zawo 7 ndipo anati kwa gulu lonse la Aisraeli, "Dziko limene tinakayendamo ndi kuliona ndi labwino kwambiri zedi. 8 Ngati Yehova akukondwera nafe, adzatitsogolera kulowa mʼdziko limenelo. Dziko loyenda mkaka ndi uchi adzalipereka kwa ife, 9 koma musawukire Yehova. Komanso musaope anthu a mʼdzikomo, pakuti tidzawagonjetsa. Chitetezo chawachokera, koma ife Yehova ali nafe. Musawaope."

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.