Pular para o conteúdo
Publicidade

Numeri 4:5,15,24,31

5 Pamene anthu akusamuka pa msasa, Aaroni ndi ana ake aamuna azilowa mu tenti ndi kuchotsa chinsalu chotchingira ndi kuphimba nacho bokosi la umboni.

15 "Aaroni ndi ana ake aamuna akamaliza kukutira ziwiya za ku malo wopatulika ndi zipangizo zopatulika zonse, ndipo akakonzeka kusamuka pamalopo, Akohati abwere kudzazinyamula koma asagwire zinthu zopatulikazo. Akatero adzafa. Izi ndizo zinthu zimene Akohati ayenera kunyamula mu tenti ya msonkhano.

24 "Ntchito ya mafuko a Ageresoni pamene akugwira ntchito ndi kunyamula katundu ndi iyi:

31 Ntchito yawo pamene azikatumikira mu tenti ya msonkhano ndi iyi: kunyamula matabwa a chihema, mitanda, mizati ndi matsinde,

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.