Moyo Watsopano mwa Khristu
1 Choncho, tsopano amene ali mwa Khristu Yesu alibe mlandu owatsutsa 2 chifukwa mwa Khristu Yesu, lamulo la Mzimu Woyera amene amapereka moyo, lawamasula ku lamulo la tchimo ndi la imfa. 3 Pakuti zimene Malamulo sanathe kuzichita, popeza anali ofowoka chifukwa cha khalidwe lathu la uchimo, Mulungu anazichita potumiza Mwana wake mʼchifanizo cha munthu ochimwa kuti akhale nsembe yauchimo. Ndipo Iye anagonjetsa tchimo mʼthupi la munthu, 4 ndi cholinga chakuti chilungamo chofunikira cha lamulo chikwaniritsidwe kwathunthu mwa ife amene sitikhala monga mwachikhalidwe chathu cha uchimo koma mwa Mzimu.
5 Pakuti anthu amene amakhala monga mwa makhalidwe oyipa a thupi amayika malingaliro awo pa zinthu zathupi. Koma amene amakhala monga mwa Mzimu amayika malingaliro awo pa zinthu za Mzimu. 6 Kuyika mtima pa zathupi ndi imfa koma kuyika mtima pa za Mzimu ndi moyo ndi mtendere. 7 Pakuti mtima umene wakhazikika pa zathupi ndi wodana ndi Mulungu. Sunagonjere lamulo la Mulungu ndipo sungathe kutero. 8 Ndipo anthu amene amalamulidwa ndi khalidwe lauchimo sangathe kukondweretsa Mulungu.
9 Koma inu simulamulidwanso ndi khalidwe lanu lauchimo koma ndi Mzimu ngati Mzimu wa Mulungu akhaladi mwa inu. Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu, iyeyu si wa Khristu.
13 Pakuti ngati inu mukhala monga mwa khalidwe lauchimo, mudzafa. Koma ngati mwa Mzimu mupha ntchito zoyipa zathupi, mudzakhala ndi moyo. 14 Onse amene amatsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu ndi ana a Mulungu.