Pular para o conteúdo
Publicidade

Aroma 8:11-17

11 Ndipo ngati Mzimu wa Mulungu amene anaukitsa Yesu kwa akufa akhala mwa inu, Iyeyo amene anaukitsa Khristu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu amene amafa kudzera mwa Mzimu wake amene amakhala mwa inu.

12 Kotero abale, ife tili ndi zoti tikwaniritse, koma osati za khalidwe lathu lauchimo, kumachita zofuna zake. 13 Pakuti ngati inu mukhala monga mwa khalidwe lauchimo, mudzafa. Koma ngati mwa Mzimu mupha ntchito zoyipa zathupi, mudzakhala ndi moyo. 14 Onse amene amatsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu ndi ana a Mulungu. 15 Mzimu amene inu munalandira samakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha, koma Mzimu amakusandutsani ana. Ndipo mwa Iye ife timafuwula kuti, "Abba, Atate." 16 Mzimu mwini amavomerezana ndi mzimu wathu kuti ife ndife ana a Mulungu. 17 Tsono ngati tili ana ake, ndiye kuti ndife olowa mʼmalo a Mulungu ndi olowa mʼmalo pamodzi ndi Khristu. Ngati ife timva zowawa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.