Kuchita Tsankho Nʼkosaloledwa
1 Abale anga, okhulupirira Yesu Khristu waulemerero, musaonetse tsankho. 2 Tangoganizirani, pakati panu patabwera munthu atavala mphete yagolide ndi zovala zapamwamba, ndipo winanso wosauka nʼkulowa atavala sanza. 3 Ngati musamala kwambiri munthu wovala bwinoyu uja, nʼkumuwuza kuti, "Khalani pa mpando wabwinowu," koma wosauka uja nʼkumuwuza kuti, "Ima apo," kapena "Khala pansi pafupi ndi chopondapo mapazi angawa," 4 kodi simunachite tsankho pakati panu ndi kukhala oweruza a maganizo oyipa?