Pular para o conteúdo
Publicidade

Yakobo 2:14-26

Chikhulupiriro ndi Ntchito Zabwino

14 Abale anga, phindu lake nʼchiyani ngati munthu anena kuti ali ndi chikhulupiriro koma chopanda ntchito zabwino? Kodi chikhulupiriro choterechi chingamupulumutse? 15 Tangoganizirani, mʼbale kapena mlongo amene ali ndi usiwa, ndipo alibe chakudya cha tsiku ndi tsiku. 16 Ngati mmodzi wa inu amuwuza kuti, "Pita ndi mtendere, ukafundidwe ndipo ukakhute," koma osamupatsa zimene akuzisowa, phindu lake nʼchiyani pamenepa? 17 Chomwechonso, chikhulupiriro chokha chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.

18 Koma wina anganene kuti, "Inuyo muli ndi chikhulupiriro koma ine ndili ndi ntchito zabwino."

Onetsani chikhulupiriro chanu chopanda ntchito zabwino ndipo ineyo ndidzakuonetsani chikhulupiriro changa pochita ntchito zabwino. 19 Mumakhulupirira kuti kuli Mulungu mmodzi yekha. Mumachita bwino. Komatu ngakhale ziwanda zimakhulupirira zimenezi ndipo zimanjenjemera ndi mantha.

20 Munthu wopusa iwe, kodi ukufuna umboni woti chikhulupiriro chopanda ntchito zabwino nʼchakufa? 21 Kodi Abrahamu kholo lathu sanatengedwe kukhala wolungama chifukwa cha zimene anachita pamene anapereka mwana wake Isake pa guwa lansembe? 22 Tsono mukuona kuti chikhulupiriro chake ndi ntchito zabwino zinkachitika pamodzi, ndipo chikhulupiriro chake chinasanduka chenicheni chifukwa cha ntchito zake zabwino. 23 Ndipo Malemba akunena kuti, "Abrahamu anakhulupirira Mulungu ndipo anatengedwa kukhala wolungama," ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu. 24 Tsono mukuona kuti munthu amasanduka wolungama ndi ntchito zabwino osati ndi chikhulupiriro chokha ayi.

25 Nʼchimodzimodzinso, kodi wadama uja, Rahabe, sanasanduke wolungama chifukwa cha zomwe anachita pamene anapereka malo ogona kwa azondi aja ndi kuwathawitsira mbali ina? 26 Monga thupi lopanda mzimu ndi lakufa, chomwechonso chikhulupiriro chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.