10 Milagres de Jesus na Bíblia: Lista com versículos e explicação
Os milagres de Jesus são muito mais do que demonstrações de poder sobrenatural; eles são sinais que confirmam sua divindade e missão. Ao longo dos Evangelhos, vemos Cristo curando enfermos, dominando a natureza e vencendo a morte.
Neste guia, selecionamos 10 milagres de Jesus na Bíblia, organizados com referências e uma breve explicação sobre o impacto espiritual de cada um deles.
Os principais milagres de Jesus nos Evangelhos
1. Transformação da Água em Vinho
Referência: João 2:1-11
Explicação: Ocorreu nas Bodas de Caná. Sendo o seu primeiro milagre público, Jesus demonstrou autoridade sobre a matéria e a natureza, revelando sua glória aos discípulos e abençoando a instituição da família.
Yesu Asandutsa Madzi Kukhala Vinyo
Pa tsiku lachitatu munali ukwati mu Kana wa ku Galileya. Amayi ake a Yesu anali komweko, ndipo Yesu ndi ophunzira ake anayitanidwanso ku ukwatiwo. Vinyo atatha, amayi a Yesu anati kwa Iye, "Wawathera vinyo."
Yesu anayankha kuti, "Amayi, chifukwa chiyani mukundiwuza Ine? Nthawi yanga sinakwane."
Amayi ake anati kwa antchito, "Inu muchite chilichonse chimene akuwuzeni."
Pamenepo panali mitsuko yamiyala yothiramo madzi isanu ndi umodzi, imene Ayuda amagwiritsa ntchito pa mwambo wodziyeretsa. Uliwonse unali ndi malita 100 kapena kupitirirapo.
Yesu anati kwa antchitowo, "Dzazani madzi mʼmitsukoyi," ndipo iwo anadzaza ndendende.
Ndipo Iye anatinso kwa iwo, "Tsopano tungani ndipo kaperekeni kwa mkulu waphwando."
Iwo anachita momwemo. Mkulu waphwando analawa madziwo amene anasandulika vinyo, ndipo sanazindikire kumene vinyoyo anachokera, ngakhale kuti antchito amene anatunga madziwo amadziwa. Kenaka anayitanira mkwati pambali ndipo anati, "Aliyense amatulutsa vinyo wokoma kwambiri poyambirira ndipo kenaka vinyo wosakoma pamene oyitanidwa atamwa kale wambiri; koma iwe wasunga wokoma mpaka tsopano."
Ichi chinali chizindikiro chodabwitsa choyamba chimene Yesu anachita ku Kana wa ku Galileya. Potero Iye anawulula ulemerero wake, ndipo ophunzira ake anamukhulupirira Iye.
2. Cura do cego de nascença
Referência: João 9:1-12
Explicação: Jesus usa lodo para curar um homem que nunca havia enxergado. Este milagre prova que Ele é a Luz do Mundo e tem poder para restaurar o que nasceu com defeito.
Yesu Achiritsa Munthu Wosaona Chibadwire
Iye akuyendabe, anaona munthu wosaona chibadwire. Ophunzira ake anamufunsa Iye kuti, "Rabi anachimwa ndani, munthuyu kapena makolo ake, kuti iye abadwe wosaona?"
Yesu anayankha kuti, "Sikuti iyeyu anachimwa kapena makolo ake, koma izi zinachitika kuti Mulungu aonetse ntchito zake mwa iyeyu. Ife tiyenera kugwira ntchito za Iye amene anandituma kukanali masana. Usiku ukubwera, pamene wina aliyense sadzagwira ntchito. Pamene Ine ndili mʼdziko lapansi, Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi."
Atanena izi, Iye anathira malovu pansi ndi kukanda dothi, napaka matopewo mʼmaso a munthuyo. Yesu anamuwuza iye kuti, "Pita kasambe mʼdziwe la Siloamu" (mawu awa akutanthauza Wotumidwa). Choncho munthuyo anapita ndi kukasamba ndipo anabwerako akupenya.
Anzake ndi iwo amene anamuona iye poyamba akupempha anafunsa kuti, "Kodi uyu si munthu amene amapemphapempha uja?" Ena ananena kuti anali yemweyo.
Ena anati, "Ayi, sakuoneka ngati yemweyo."
Koma iye mwini ananenetsa kuti, "Munthuyo ndine."
Iwo anafunsitsa kuti, "Kodi nanga maso ako anatsekuka bwanji?"
Iye anayankha kuti, "Munthu wina wotchedwa Yesu anakanda dothi ndi kupaka mʼmaso anga. Iye anandiwuza kuti ndipite ku Siloamu ndi kukasamba. Choncho ndinapita kukasamba, ndipo ndikuona."
Iwo anamufunsa iye kuti, "Ali kuti munthu ameneyu?"
Iye anati, "Ine sindikudziwa."
3. Multiplicação dos pães e peixes
Referência: Mateus 14:13-21
Explicação: Com apenas cinco pães e dois peixes, Jesus alimentou mais de 5 mil homens. Este sinal revela Cristo como o Pão da Vida, aquele que supre todas as nossas necessidades.
Yesu Adyetsa Anthu 5,000
Yesu atamva zimene zinachitika, anachoka pa bwato mwachinsinsi kupita kumalo a yekha. Magulu a anthu atamva izi anamutsatira Iye poyenda pansi kuchokera ku mizinda. Yesu atafika ku mtunda, ndi kuona gulu lalikulu la anthu, Iye anamva nawo chifundo ndipo anachiritsa odwala awo.
Kutayamba mdima, ophunzira anabwera kwa Iye nati, "Kuno ndi kutchire ndipo kwayamba kale kuda. Awuzeni anthu azipita kuti afike ku midzi ndi kukadzigulira zakudya."
Yesu anawayankha kuti, "Sikofunika kuti azipita. Inuyo muwapatse kanthu kuti adye."
Iwo anayankha kuti, "Tili ndi malofu asanu okha a buledi ndi nsomba ziwiri."
Koma Iye anati, "Bweretsani kwa Ine." Analamula anthu kuti akhale pansi pa udzu ndipo anatenga buledi musanu ndi nsomba ziwiri nayangʼana kumwamba, nayamika nagawa bulediyo. Kenaka anapereka bulediyo kwa ophunzira ake ndipo ophunzirawo anagawira anthu. Onse anadya nakhuta ndipo ophunzira anatola zotsalira ndi kudzaza madengu khumi ndi awiri. Chiwerengero cha amene anadya kupatulako amayi ndi ana chinali pafupifupi amuna 5,000.
4. Jesus acalma a tempestade
Referência: Marcos 4:35-41
Explicação: Com uma ordem, o vento e o mar se aquietam. O milagre ensina sobre a paz que excede o entendimento e a autoridade do Messias sobre a criação.
Yesu Aletsa Namondwe
Tsiku limenelo atafika madzulo, anawuza ophunzira ake kuti, "Tiyeni tiwolokere tsidya lina." Atasiya gulu la anthu mʼmbuyo, anamutenga Iye, napita naye monga momwe anali mʼbwatolo. Panalinso mabwato ena pamodzi ndi Iye. Mphepo yamkuntho inabuka, ndipo mafunde anawomba bwatolo, kotero kuti linali pafupi kumira. Pa nthawi imeneyi Yesu anali akugona atatsamira pilo kumbuyo kwa bwato. Ophunzira anamudzutsa nati kwa Iye, "Aphunzitsi, kodi simukusamala kuti timira?"
Yesu anauka nadzudzula mphepo nati kwa mafunde, "Chete! Khala bata!" Pamenepo mphepo inaleka ndipo kunachita bata.
Iye anati kwa ophunzira ake, "Muli ndi mantha chifukwa chiyani? Kodi mukanalibe chikhulupiriro?"
Iwo anachita mantha nafunsana wina ndi mnzake kuti, "Uyu ndani? Ngakhale mphepo ndi nyanja zimumvera Iye!"
5. Cura da mulher com fluxo de sangue
Referência: Marcos 5:25-34
Explicação: Uma cura que aconteceu pelo toque da fé. Jesus mostra que está atento ao sofrimento individual e que a fé é o canal para receber o milagre.
Pomwepo panali mayi amene amadwala nthenda yotaya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri. Iye anavutika kwambiri pamene asingʼanga ambiri ankamusamalira ndipo anagwiritsa ntchito zonse anali nazo, koma mʼmalo mochira, nthenda yake inkakulakulabe. Atamva za Yesu, anabwera kumbuyo kwake mʼgulu la anthu ndipo anakhudza mkanjo wake, chifukwa anaganiza kuti, "Ngati nditangokhudza mkanjo wake, ndidzachiritsidwa." Nthawi yomweyo magazi ake analeka kutuluka ndipo anamva mʼthupi mwake kuti wamasulidwa ku vuto lake.
Pomwepo Yesu anazindikira kuti mphamvu inachoka mʼthupi mwake. Anatembenuka mʼgulu la anthu ndipo anafunsa kuti, "Ndani wakhudza zovala zanga?"
Ophunzira ake anayankha kuti, "Mukuona kuti anthu akukupanikizani, ndipo Inu mukufunsa kuti, ‘Ndani wandikhudza?’ "
Koma Yesu anapitirizabe kuyangʼana kuti aone amene anachita zimenezi. Kenaka mayi uja pozindikira chimene chinamuchitikira, anabwera ndi kugwa pa mapazi ake, ndipo akunjenjemera ndi mantha, anamuwuza zoona zokhazokha. Anati kwa iye, "Mwana wamkazi, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere ndipo khala womasulidwa ku mavuto ako."
6. Libertação do endemoninhado Gadareno
Referência: Marcos 5:1-20
Explicação: Jesus liberta um homem dominado por uma legião de espíritos. É a prova clara de sua autoridade absoluta sobre o reino das trevas.
Yesu Achiritsa Wogwidwa ndi Ziwanda
Ndipo anawoloka nyanja napita ku dera la Gerasa. Yesu atatuluka mʼbwato, munthu amene anali ndi mzimu woyipa anachoka ku manda ndi kukumana naye. Munthuyu amakhala ku manda, ndipo panalibe amene akanatha kumumanganso ngakhale ndi unyolo. Pakuti nthawi zambiri akamumanga manja ndi miyendo amadula maunyolo ndi kudula zitsulo zimene zinali mʼmapazi ake. Panalibe amene anali ndi mphamvu yoti ndi kumugonjetsa. Usana ndi usiku ankakhala ku manda ndi kumapiri, akulira ndi kudzicheka ndi miyala.
Ataona Yesu ali patali, anathamanga nagwa pa mawondo ake pamaso pake. Iye anafuwula kwambiri nati, "Mukufuna muchite nane chiyani, Yesu Mwana wa Mulungu Wammwambamwamba? Lumbirani kwa Mulungu kuti simundizunza!" Pakuti Yesu anati kwa iye, "Tuluka mwa munthuyu, iwe mzimu woyipa!"
Ndipo Yesu anamufunsa iye, "Dzina lako ndani?"
Iye anayankha kuti, "Dzina langa ndine Legiyo, pakuti tilipo ambiri." Ndipo anamupempha Yesu mobwerezabwereza kuti asazitulutse mʼderalo.
Gulu lalikulu la nkhumba limadya mʼmbali mwa phiri limene linali pafupi. Ziwandazo zinapempha Yesu kuti, "Titumizeni pakati pa nkhumbazo; ndipo mutilole tilowe mwa izo." Iye anazipatsa chilolezo, ndipo mizimu yoyipayo inatuluka ndi kukalowa mu nkhumbazo. Gulu la nkhumba, zokwana pafupifupi 2,000 zinathamanga kutsetserekera ku nyanja ndipo zinamira.
Omwe amaweta nkhumbazo anathawa ndi kukawuza anthu za izi mu mzinda ndi ku madera a ku midzi, ndipo anthu anapita kukaona zomwe zinachitika. Atafika kwa Yesu, anaona munthu amene anagwidwa ndi ziwanda zambiri uja atakhala pansi pomwepo, atavala, ndipo ali bwinobwino. Iwo anachita mantha. Amene anaona zimenezi anawuza anthu zomwe zinachitika kwa munthu wogwidwa ndi ziwandayo ndipo anawawuzanso za nkhumbazo. Ndipo anthu anayamba kumupempha Yesu kuti achoke mʼdera lawo.
Yesu akulowa mʼbwato, munthu amene anagwidwa ndi ziwanda uja anamupempha kuti apite nawo. Yesu sanamulole, koma anati, "Pita kwanu ku banja lako ndipo ukawawuze zimene Ambuye wakuchitira, ndi chifundo chimene wakuchitira." Pomwepo munthuyo anapita nayamba kuwuza anthu a ku Dekapoli zinthu zimene Yesu anamuchitira. Ndipo anthu onse anadabwa.
7. Ressurreição da filha de Jairo
Referência: Marcos 5:21-43
Explicação: Jesus demonstra que a morte para Ele é como o sono. Ele restaura a vida de uma criança, trazendo esperança para uma família desesperada.
Mtsikana Womwalira ndi Mayi Wodwala
Yesu atawolokeranso pa bwato kupita mbali ina ya nyanja, gulu lalikulu la anthu linasonkhana momuzungulira. Ali mʼmbali mwa nyanja, mmodzi wa akulu a mʼsunagoge, dzina lake Yairo anafika pamenepo. Ataona Yesu, anagwa pa mapazi ake, ndi kumudandaulira kwambiri nati, "Mwana wanga wamkazi wamngʼono ali pafupi kufa. Chonde tiyeni kuti mukamusanjike manja kuti akachiritsidwe nakhala ndi moyo." Ndipo Yesu anapita naye.
Gulu lalikulu la anthu linamutsata ndi kumamupanikiza Iye. Pomwepo panali mayi amene amadwala nthenda yotaya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri. Iye anavutika kwambiri pamene asingʼanga ambiri ankamusamalira ndipo anagwiritsa ntchito zonse anali nazo, koma mʼmalo mochira, nthenda yake inkakulakulabe. Atamva za Yesu, anabwera kumbuyo kwake mʼgulu la anthu ndipo anakhudza mkanjo wake, chifukwa anaganiza kuti, "Ngati nditangokhudza mkanjo wake, ndidzachiritsidwa." Nthawi yomweyo magazi ake analeka kutuluka ndipo anamva mʼthupi mwake kuti wamasulidwa ku vuto lake.
Pomwepo Yesu anazindikira kuti mphamvu inachoka mʼthupi mwake. Anatembenuka mʼgulu la anthu ndipo anafunsa kuti, "Ndani wakhudza zovala zanga?"
Ophunzira ake anayankha kuti, "Mukuona kuti anthu akukupanikizani, ndipo Inu mukufunsa kuti, ‘Ndani wandikhudza?’ "
Koma Yesu anapitirizabe kuyangʼana kuti aone amene anachita zimenezi. Kenaka mayi uja pozindikira chimene chinamuchitikira, anabwera ndi kugwa pa mapazi ake, ndipo akunjenjemera ndi mantha, anamuwuza zoona zokhazokha. Anati kwa iye, "Mwana wamkazi, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere ndipo khala womasulidwa ku mavuto ako."
Pamene Yesu ankayankhulabe, amuna ena anafika kuchokera ku nyumba ya Yairo, mkulu wa sunagoge. Iwo anati, "Mwana wanu wamkazi wamwalira, muvutitsiranjinso aphunzitsiwa?"
Posasamala zomwe ananena, Yesu anamuwuza mkulu wa sunagoge uja kuti, "Usachite mantha; ingokhulupirira."
Iye sanalole munthu wina aliyense kuti amutsatire koma Petro, Yakobo ndi Yohane mʼbale wa Yakobo. Atafika ku nyumba ya mkulu wa sunagoge, Yesu anaona chipiringu cha anthu akulira ndi kufuwula kwambiri. Analowa nati kwa iwo, "Mukuchita phokoso ndi kulira chifukwa chiyani? Mwanayu sanamwalire koma ali mtulo." Koma anamuseka Iye.
Atawatulutsa onse panja, Iye anatenga abambo ndi amayi ake a mwanayo ndi ophunzira omwe anali naye, ndipo analowa mʼmene munali mwanayo. Anagwira dzanja lake nanena kwa iye, "Talita Kumi!" (Kutanthauza kuti, "Mtsikana, ndikunena ndi iwe, imirira!") Nthawi yomweyo anayimirira nayenda mozungulira (anali wa zaka khumi ndi ziwiri). Pa ichi onse anadabwa kwambiri. Anawalamulira kwambiri kuti asawuze wina aliyense za ichi, ndipo anawawuza kuti amupatse kanthu koti adye.
8. Jesus anda sobre as águas
Referência: Mateus 14:22-33
Explicação: Ao caminhar sobre o Mar da Galileia, Jesus mostra que não está sujeito às leis da física. O episódio também serve para tratar a fé e a dúvida no coração de Pedro.
Yesu Ayenda pa Nyanja
Nthawi yomweyo anawawuza ophunzira ake kuti alowe mʼbwato ndi kuti atsogole kupita kutsidya lina pamene Iye ankawuza anthu kuti azipita kwawo. Atatha kuwawuza kuti azipita kwawo, Iye anakwera ku phiri yekha kukapemphera. Pamene kumada anali kumeneko yekha. Pamenepo nʼkuti bwato litapita patali pangʼono kuchokera ku mtunda ndipo linavutika ndi mafunde chifukwa mphepo inkawomba mokumana nalo.
Pa ora lachinayi usiku, Yesu anabwera kwa iwo akuyendabe pa nyanja. Ophunzira atamuona akuyenda pa nyanja, anaopa nati, "Ndi mzukwa!" Ndipo analira chifukwa cha mantha.
Koma Yesu nthawi yomweyo anawawuza kuti, "Limbani mtima! Ndine, musaope."
Petro anayankha nati, "Ambuye ngati ndinu, mundiwuze ndibwere kuli inuko pa madzipo."
Iye anati, "Bwera."
Pamenepo Petro anatuluka mʼbwato ndipo anayenda pa madzi kupita kwa Yesu. Koma ataona mphepo, iye anachita mantha ndipo anayamba kumira, nafuwula nati, "Ambuye ndipulumutseni!"
Ndipo mofulumira Yesu anatambasula dzanja lake namugwira iye, nati, "Iwe wachikhulupiriro chochepa, bwanji unakayika?"
Ndipo atalowa mʼbwato mphepo inaleka. Pamenepo amene anali mʼbwato anamulambira Iye, nati, "Zoonadi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu."
9. Cura do paralítico
Referência: Marcos 2:1-12
Explicação: Jesus cura o corpo, mas primeiro perdoa os pecados. Este milagre estabelece que sua missão principal é a reconciliação espiritual do homem com Deus.
Yesu Achiritsa Munthu Wofa Ziwalo
Patapita masiku pangʼono, Yesu atalowanso mu Kaperenawo, zinamveka kuti wabwera ali mʼnyumba. Choncho anthu ambiri anasonkhana kotero kuti panalibenso malo, ngakhale ndi pa khomo pomwe, ndipo Iye anawalalikira mawu. Amuna anayi anabwera, atanyamula munthu wofa ziwalo. Popeza sakanatha kufika naye kwa Yesu chifukwa cha gulu la anthu, anasasula denga chapamwamba pamene panali Yesu, ndipo atabowoleza, anatsitsa mphasa yomwe munthu wofa ziwaloyo anagonapo. Yesu ataona chikhulupiriro chawo, anati kwa wofa ziwaloyo, "Mwana, machimo ako akhululukidwa."
Ndipo ena mwa aphunzitsi amalamulo anakhala pansi pomwepo, namaganiza mʼmitima mwawo kuti, "Nʼchifukwa chiyani munthuyu ayankhula chotere? Iye akuchitira mwano Mulungu! Ndani angakhululukire munthu machimo kupatula Mulungu yekha?"
Nthawi yomweyo Yesu anadziwa mu mzimu wake kuti izi ndi zimene ankaganiza mʼmitima yawo, ndipo anawawuza kuti, "Chifukwa chiyani mukuganiza zinthu izi? Chapafupi nʼchiyani; kunena kwa wofa ziwaloyu kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kuti, ‘Imirira, tenga mphasa yako ndipo yenda?’ Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko lapansi wokhululukira machimo." Anati kwa wofa ziwaloyo, "Ndikuwuza iwe, imirira, tenga mphasa yako ndipo pita kwanu." Anayimirira, nanyamula mphasa yake natuluka onse akumuona. Izi zinadabwitsa aliyense ndipo anayamika Mulungu nati, "Sitinaonepo zinthu ngati izi!"
10. Ressurreição de Lázaro
Referência: João 11:1-44
Explicação: O milagre mais impactante antes da crucificação. Ao ressuscitar alguém morto há quatro dias, Jesus declara: "Eu sou a ressurreição e a vida".
Imfa ndi Kuukitsidwa kwa Lazaro
Tsopano munthu wina dzina lake Lazaro anadwala. Iye anali wa ku Betaniya, mudzi wa Mariya ndi mchemwali wake Marita. Mariyayo ndi yemwe uja amene anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake. Lazaro wodwalayo anali mlongo wake. Choncho alongo ake anatumiza mawu kwa Yesu kuti, "Ambuye, uja amene Inu mumamukonda akudwala."
Atamva izi, Yesu anati, "Kudwalako safa nako. Koma akudwala kuti Mulungu alemekezedwe; ndi kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe chifukwa cha matendawo." Yesu anakonda Marita, mchemwali wake ndi Lazaro. Koma atamva kuti Lazaro akudwala, Iye anakhalabe kumene anali masiku ena awiri.
Kenaka anati kwa ophunzira ake, "Tiyeni tibwerere ku Yudeya."
Ophunzira akewo anati, "Rabi, posachedwa pomwepa Ayuda anafuna kukugendani ndi miyala, koma Inu mukupitanso komweko?"
Yesu anayankha kuti, "Kodi sipali maora khumi ndi awiri pa tsiku? Munthu amene amayenda masana sapunthwa, popeza akuona chifukwa cha kuwala kwa dziko lapansi. Koma amene akuyenda usiku amapunthwa, chifukwa kuwalako alibe."
Iye atatha kunena izi, anapitirira kuwawuza iwo kuti, "Bwenzi lathu Lazaro wagona tulo; koma Ine ndikupita kumeneko kukamudzutsa."
Ophunzira ake anayankha kuti, "Ambuye, ngati wagona adzapeza bwino." Yesu ankayankhula za imfa yake koma ophunzira ake ankaganiza kuti amanena za tulo chabe.
Ndipo kenaka anawawuza momveka kuti, "Lazaro wamwalira. Ine ndikukondwera chifukwa cha inu kuti kunalibe kumeneko; koma kuti mukakhulupirire tiyeni tipiteko."
Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, anati kwa ophunzira anzake, "Tiyeni nafenso tipite, kuti tikafere naye pamodzi."
Yesu Atonthoza Alongo a Lazaro
Yesu atafika, anapeza kuti Lazaro anali atagona mʼmanda masiku anayi. Mudzi wa Betaniya unali pafupi ndi Yerusalemu pa mtunda wosachepera makilomita atatu, ndipo Ayuda ambiri anabwera kwa Marita ndi Mariya kudzawatonthoza pa imfa ya mʼbale wawo. Pamene Marita anamva kuti Yesu akubwera, anapita kukakumana naye. Koma Mariya anatsala ku nyumba.
Marita anati kwa Yesu, "Ambuye, mukanakhala muli kuno, mlongo wanga sakanamwalira. Koma ine ndikudziwa kuti ngakhale tsopano Mulungu adzakupatsani chilichonse chimene mudzamupempha."
Yesu anati kwa iye, "Mlongo wako adzauka."
Marita anayankha kuti, "Ine ndikudziwa kuti adzauka pa kuukanso pa tsiku lomaliza."
Yesu anati kwa iye, "Ine ndine kuuka ndi moyo. Wokhulupirira Ine, angakhale amwalira adzakhala ndi moyo. Aliyense amene ali ndi moyo ndi kukhulupirira Ine sadzamwalira. Kodi iwe ukukhulupirira izi?"
Marita anamuwuza Iye kuti, "Inde Ambuye, ine ndikukhulupirira kuti ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu, amene abwera mʼdziko lapansi."
Ndipo iye atanena izi anabwerera ndi kukayitana mchemwali wake Mariya namuyankhula monongʼona pambali, nati, "Aphunzitsi abwera ndipo akukuyitana." Mariya atamva izi, anayimirira mofulumira napita kwa Iye. Tsopano nʼkuti Yesu asanalowe mʼmudzi, koma anali akanali pa malo pamene Marita anakumana naye. Ayuda amene ankamutonthoza Mariya mʼnyumba, anaona mmene iye anayimira mofulumira ndi kutuluka kunja, iwo anamutsata akuganizira kuti ankapita ku manda kukalirira kumeneko.
Mariya anafika pamalo pamene panali Yesu ndipo atamuona, anagwa pa mapazi ake ndipo anati, "Ambuye mukanakhala muli kuno mlongo wanga sakanamwalira."
Yesu ataona iye akulira, ndi Ayuda amene anabwera naye akuliranso, anakhudzidwa kwambiri ndi kuvutika mu mzimu. Iye anafunsa kuti, "Kodi mwamuyika kuti?"
Iwo anayankha kuti, "Ambuye tiyeni mukaone."
Yesu analira.
Pamenepo Ayuda anati, "Taonani mmene Iye anamukondera Lazaro!"
Koma ena a iwo anati, "Iye amatsekula maso a munthu wosaona, kodi sakanakhoza kuletsa kuti munthu uyu asamwalire?"
Yesu Aukitsa Lazaro
Yesu atakhudzidwanso kwambiri anafika ku manda. Manda akewo anali phanga ndipo anatsekapo ndi mwala. Yesu anati, "Chotsani mwala."
Marita mlongo wa womwalirayo anati, "Koma Ambuye, nthawi ino wayamba kununkha, pakuti wakhala mʼmenemu masiku anayi."
Kenaka Yesu anati, "Kodi Ine sindinakuwuze kuti ngati iwe ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?"
Choncho iwo anachotsa mwalawo. Kenaka Yesu anayangʼana kumwamba ndikuti, "Atate, Ine ndikukuthokozani chifukwa mumandimvera. Ine ndimadziwa kuti Inu mumandimvera nthawi zonse, koma Ine ndanena izi chifukwa cha anthu amene ayima pano, kuti iwo akhulupirire kuti Inu munandituma Ine."
Yesu atanena izi, Iye anayitana ndi mawu ofuwula kuti, "Lazaro, tuluka!" Munthu womwalirayo anatuluka, womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za ku manda, ndi nkhope yake yokulungidwa nsalu.
Yesu anawawuza kuti, "Mʼmasuleni, ndipo muloleni apite."
Conclusão
Os milagres de Jesus revelam sua autoridade sobre a natureza, as enfermidades, o mundo espiritual e até a morte. Eles não são apenas demonstrações de poder, mas sinais que apontam para sua identidade e missão.
Ao estudar esses milagres, é possível compreender melhor o papel de Jesus e a mensagem central do Evangelho.
Se este conteúdo ajudou você a entender os milagres de Jesus na Bíblia, compartilhe este artigo para que mais pessoas também conheçam esses ensinamentos.