Pular para o conteúdo
Publicidade

A fé vem pelo ouvir

Por Bíblia Online

A fé vem pelo ouvir, e o ouvir pela Palavra de Cristo. Quando a Palavra é proclamada, a fé nasce nos corações. Ouvir a Deus é o primeiro passo para crer e seguir.

A fé vem pelo ouvir

A fé vem pelo ouvir, e o ouvir pela Palavra de Cristo. Quem ouve a Palavra crê e obtém a salvação eterna.

Pakuti palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina, pakuti Ambuye mmodzi yemweyo ndi Ambuye wa onse ndipo amadalitsa mochuluka onse amene ayitana pa Iye pakuti, "Aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka."

Kodi adzayitana bwanji amene sanamukhulupirire? Ndipo adzakhulupirira bwanji asanamve za Iye? Ndipo adzamva bwanji popanda wina kulalikira kwa iwo? Ndipo iwo adzalalikira bwanji osatumidwa? Kwalembedwa kuti, "Akongoladi mapazi a iwo amene amabweretsa Uthenga Wabwino!"

Koma si onse amene anavomereza Uthenga Wabwino. Pakuti Yesaya akuti, "Ambuye, ndani amene wakhulupirira uthenga wathu?" Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu.

Ine ndikufuna ndiphunzire kuchokera kwa inu chinthu chimodzi ichi: Kodi munalandira Mzimu pochita ntchito za lamulo, kapena pokhulupirira zimene munamva?

Ndipo inunso pamene munamva mawu a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, munayikidwanso mwa Khristu. Mutakhulupirira, anakusindikizani chizindikiro pokupatsani Mzimu Woyera amene Iye analonjeza. Mzimu Woyerayo ndi chikole chotsimikizira kuti tidzalandira madalitso athu, ndipo kuti Mulungu anatiwombola kuti tikhale anthu ake. Iye anachita zimenezi kuti timuyamike ndi kumulemekeza.

"Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo.

Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano, pamene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu ndipo iwo amene amva adzakhala ndi moyo.

Palibe munthu amene angabwere kwa Ine, ngati Atate amene anandituma Ine samubweretsa. Ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. Aneneri analemba kuti, "Onse adzaphunzitsidwa ndi Mulungu! Aliyense amene amamva Atate ndi kuphunzira kwa Iye amabwera kwa Ine. Palibe amene anaona Atate koma yekhayo amene achokera kwa Mulungu; yekhayo ndiye anaona Atate. Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Iye amene akhulupirira ali nawo moyo wosatha.

Ouvir e obedecer

Felizes os que ouvem a Palavra de Deus e a praticam. Quem tem ouvidos ouça o que o Espírito diz.

Koma Yesu anayankha kuti, "Odala ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kuwasunga."

Ngati wina ali ndi makutu akumva, amve."

Anati kwa iwo, "Pitani mʼdziko lonse lapansi ndipo mukalalikire Uthenga Wabwino kwa zolengedwa zonse.

Mwa iwo zimene ananenera Yesaya zikwaniritsidwa:

" Kumva mudzamva koma osamvetsetsa.

Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu.

Pakuti mtima wa anthu awa ndi wokanika,

mʼmakutu mwawo ndi mogontha,

ndipo atsinzina

kuti asaone kanthu.

Mwina angapenye ndi maso awo,

angamve ndi makutu awo, angamvetse ndi nzeru zawo ndi kutembenuka,

Ineyo nʼkuwachiritsa.

Koma maso anu ndi odala chifukwa amapenya ndi makutu anu chifukwa amamva.

Yesu anayitana gulu la anthu nati, "Mverani ndipo zindikirani.

Tcherani makutu ndipo mubwere kwa Ine;

mvereni Ine, kuti mukhale ndi moyo.

Ndidzachita nanu pangano losatha,

chikondi changa chija chosasinthika ndi chodalirika ndinalonjeza Davide.

Yehova anati, "Pita ndipo ukawawuze anthu awa:

" Kumva muzimva, koma osamvetsetsa;

kupenya muzipenya koma osaona kanthu.

Tsono anthu amenewa uwaphe mtima;

uwagonthetse makutu,

ndipo uwatseke mʼmaso.

Mwina angaone ndi maso awo,

angamve ndi makutu awo,

angamvetse ndi mitima yawo,

kenaka ndi kutembenuka mtima ndi kuchiritsidwa."

Ndipo muzitipemphereranso ife kuti Mulungu atitsekulire khomo la uthenga wathu, kuti tilalikire chinsinsi cha Khristu, chimene ndine womangidwa nacho mʼndende.

Seja o primeiro