Pular para o conteúdo
Publicidade

A última palavra vem do Senhor

Por Bíblia Online

A última palavra pertence ao Senhor. Os planos do homem estão sujeitos à soberania de Deus. Ele rege toda a história e nenhum de seus propósitos pode ser frustrado.

Zolinga za mu mtima ndi za munthu,

koma kwa Yehova ndiye kumachokera yankho.

Yehova amachita zonse ndi cholinga chake,

ngakhale anthu oyipa kuti aone tsiku latsoka.

Mulungu si munthu kuti aname,

kapena mwana wa munthu kuti asinthe maganizo ake.

Kodi amayankhula koma osachita?

Kodi amalonjeza koma osakwaniritsa?

Yehova anayankha Mose kuti, "Kodi dzanja langa ndi lalifupi? Uwona tsopano ngati zimene ndanenazo zichitike kapena ayi."

Ndi mmenenso amachitira mawu ochokera mʼkamwa mwanga.

Sadzabwerera kwa Ine kopanda phindu lake,

koma adzachita zonse zimene ndifuna,

ndipo adzakwaniritsa cholinga chimene ndinawatumira.

"Taonani, Ine ndine Yehova, Mulungu wa anthu onse. Kodi chilipo chinthu choti Ine nʼkundikanika?

"Ndikudziwa kuti Inu mungathe kuchita zinthu zonse;

chimene mufuna kuchita wina sangaletse konse.

Yehova amachita chilichonse chimene chimamukomera,

kumwamba ndi dziko lapansi,

ku nyanja zazikulu ndi ku malo ake onse akuya.

Iyeyo analipo zinthu zonse zisanalengedwe ndipo zinthu zonse zimamangika pamodzi mwa Iye.

Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha."

Zikubwera! Ndipo zidzachitikadi, ndikutero Ine Ambuye Yehova. Ndiye tsiku limene ndinanena lija.

Chifukwa chiyani mukutero? Inu simukudziwa zimene ziti zichitike mawa. Kodi moyo wanu ndi wotani? Inu muli ngati nkhungu imene imangooneka kwa kanthawi kochepa ndipo kenaka ndikuzimirira. Koma inuyo muyenera kunena kuti, "Ambuye akalola, tikadzakhala ndi moyo, tidzachita zakutizakuti."

Seja o primeiro